NEWCONNECT MALAWI-DVM
NewConnect Malawi - DVM

Ali chithunzimu ndi wakuba ndipo Ali mu galimoto ya apolisi.. Uthenga wa pa 25 January 2025, uku ndi ku blantyre Chichiri, mwana wa school pa Malawi University of business and applied sciences kufwambidwa. Uthenga unali chonchi "Ma guy tagwira okuba awiri pa chichiri stage. Student mzathu wa EH2 (APATSA GEORGE) amachoka kwao ku Lilongwe anali akungofika kumene. Okubawo analipo four omwe anamulanda ndalama ndi phone. Kenako okuba aja anathawa koma katundu wina sanatenge (Laptop bag, ufa, ndi bag ya zovala). Izi zinapangisa kuti student yo apeze mpata onyamula katundu wakeyo wosalayo mkuyamba liwiro lothawira ku hostel koma tsoka ilo anakumaso ndi okuba ena analipo awiri omwe anamulanda bag yazovala, ndi ufa koma laptop bag sanatenge. Atafika ku hostel ndikuza ma guys tinanyamuka mkupita mu high way pomwe tinagwira okuba awiri. Okuba winayo wapezeka ndi phone ndi Student ID. Zinthu zinazo sitinazipeze."
![[NewConnect Malawi (27/01/2025),Wolemba :Charles Yeau Nedie]. Bwalo la milandu la Magistrate ku Lilongwe layimitsa kaye mlandu mpaka pa 20 February omwe ukukhudza Tamia Ja msungwana odziwika bwino mmasamba a mchezo popeza aboma sanapereke zikalata za mlandu ku bwaloli. Yemwe akuyimira oganiziridwayu a Stanley Chirwa adandaula kuti a kumbali ya boma sanapereke zikalatazi kwa oganiziridwa kuti akhale odziwa zomwe akubwelera ku bwaloli asanayambe kuyankhapo kotero iwo ndi omwe anapempha bwalo kuti apatsidwe nthawi. A chirwa apemphaso aboma kuti apereke zikalatazi kwa iwo pasanathe masiku asanu ndi awiri.](images/th/sd_67974e67807d2.jpg?no_cache=1737972963)
[NewConnect Malawi (27/01/2025),Wolemba :Charles Yeau Nedie]. Bwalo la milandu la Magistrate ku Lilongwe layimitsa kaye mlandu mpaka pa 20 February omwe ukukhudza Tamia Ja msungwana odziwika bwino mmasamba a mchezo popeza aboma sanapereke zikalata za mlandu ku bwaloli. Yemwe akuyimira oganiziridwayu a Stanley Chirwa adandaula kuti a kumbali ya boma sanapereke zikalatazi kwa oganiziridwa kuti akhale odziwa zomwe akubwelera ku bwaloli asanayambe kuyankhapo kotero iwo ndi omwe anapempha bwalo kuti apatsidwe nthawi. A chirwa apemphaso aboma kuti apereke zikalatazi kwa iwo pasanathe masiku asanu ndi awiri.
![[NewConnect Malawi (27/01/2025),Wolemba :Charles Yeau Nedie] kampani ina youmba nsalu ikupanga nsalu yatsopano yomwe pali nkhope ya wachiwiri kwa mtsogoleri wadzikolino Dr Michael Usi ndipo nsaluyi ayilemba kuti](images/th/sd_679758c50e207.jpg?no_cache=1737975582)
[NewConnect Malawi (27/01/2025),Wolemba :Charles Yeau Nedie] kampani ina youmba nsalu ikupanga nsalu yatsopano yomwe pali nkhope ya wachiwiri kwa mtsogoleri wadzikolino Dr Michael Usi ndipo nsaluyi ayilemba kuti "odya zake alibe mulandu". Izi zikudza pomwe pali mpheketsera kuti wachiwiri kwa mtsogoleri wadzikolino yu yemwenso anakhalapo mtsogoleri wa UTM akufuna kuyambitsa chipanichake kutsatira kuchotsedwa kwake mu chipani cha UTM.
Boma kudzera mu unduna wa zomangamanga ndi chitukuko cha dziko wati umanga nsika pafupi ndi Malawi University of business and applied sciences

30/01/2025 (by CHARLES YEAU NEDIE) Thupi la Fortune Milazie, yemwe anali ophunzira pa sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Sciences (MUBAS) lalowa m'manda Lero ku mudzi kwawo kwa Sani, mfumu yayikulu Malengachanzi m'boma la Nkhotakota. Fortune wamwalira dzulo pa chipatala cha Kamuzu Central ku Lilongwe atadwala nthawi yayitali nthenda yongotha magazi (aplastic anemia). Kunali mfuwu pomwe thupi la Fortune limalowa m'manda kwa aanthu ochuluka kuphatikizapo ogwira ntchito zaboma, akuluakulu ndi ophunzira pa sukulu ya MUBAS komanso ophunzira a sekondale yomwe Fortune anaphunzira ya Bishop Mtekateka Private. Fortune wamwalira akuyembekezeka kukalandira thandizo la chipatala ku India kutsatira kupezeka kwa ndalama yomwe imafunika kuti iye athe kupita ku m'dzikolo. Wolemba Innocent Chunga#Times360Malawi Thupi la Fortune Milazie, yemwe anali ophunzira pa sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Sciences (MUBAS) lalowa m'manda Lero ku mudzi kwawo kwa Sani, mfumu yayikulu Malengachanzi m'boma la Nkhotakota. Fortune wamwalira dzulo pa chipatala cha Kamuzu Central ku Lilongwe atadwala nthawi yayitali nthenda yongotha magazi (aplastic anemia). Kunali mfuwu pomwe thupi la Fortune limalowa m'manda kwa aanthu ochuluka kuphatikizapo ogwira ntchito zaboma, akuluakulu ndi ophunzira pa sukulu ya MUBAS komanso ophunzira a sekondale yomwe Fortune anaphunzira ya Bishop Mtekateka Private. Fortune wamwalira akuyembekezeka kukalandira thandizo la chipatala ku India kutsatira kupezeka kwa ndalama yomwe imafunika kuti iye athe kupita ku m'dzikolo.